Released on September 29, 2019

Thumbnail

[Intro: Onesimus]

(Sley)

Mm

Eh-eh, yeah

Tata-lala-ta


[Chorus: Onesimus]

Uyike mtima pansi

Usadandawule khala pansi

Zonse ndi nthawi basi

Usamasweke mtima nzinthu zazing'ono

Gwada Yehova akugwire nkono

Tadekha, tadekha

Ah

Ooh


[Verse 1: Gwamba]

Uh, gwada kwa ambuye ndi mavuto ako

Akafuna kuyankha samafunsa nzako

Muwuze zonse zokhumba za mtima wako no

Ndiwamkulu heavy kuposa vuto lako, aish

Ndiyekhayo yemwe angakukonze

Anawolotsa nyanja achina Mose

Akhale patsogolo nzinthu zonse

Olo utachimwa bwanji akudzodze

Osadanda mphwanga izi nzazing'ono

Yehova wa kumwamba ali ndi chisomo

Ika manja m'mwamba akugwire nkono (Akugwire nkono)to


[Chorus: Onesimus]

Uyike mtima pansi

Usadandawule khala pansi

Zonse ndi nthawi basi

Usamasweke mtima nzinthu zazing'ono

Gwada Yehova akugwire nkono

Tadekha, tadekha

Ah

Ooh


[Verse 2: Gwamba]

Uh, mwetulira mphwanga usanyatsitse nkhope

Akachedwa kuyankha usatope

Umawerеnga Bible, ana a mulungu anayenda pansi kwa zaka forty

Mlaliki pa guwa kulalikira a gonthi

Maso patsogolo iwe si mkazi wa loti

Pa nyanja yamachimo upangе float ngati boat

Machimo mu mtima mwako kupanga deport

Eish, mphepo ya ukali

Yawe akugwira nkono ufika kutali

Ndati mphepo ya ukali

Akayendetsa Yawe moyo wako wa utali


[Chorus: Onesimus]

Uyike mtima pansi

Usadandawule khala pansi

Zonse ndi nthawi basi

Usamasweke mtima nzinthu zazing'ono

Gwada Yehova akugwire nkono

Tadekha, tadekha

Ah

Ooh